62 episodes

Sermons and teaching in Chichewa and English from the ministry of Gospel Life Baptist Mission.

Chiphunzitso Choona | Sound Doctrine from Gospel Life Gospel Life Baptist Mission

  • Religion & Spirituality

Sermons and teaching in Chichewa and English from the ministry of Gospel Life Baptist Mission.

  Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu/God is greater than our hearts

  Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu/God is greater than our hearts

  1 Yohane 3:19-24, kulimbika mtima pamaso pa mulungu kumathandiza ife kuzindikira kuti tili pa choonadi ndipo timakhala okhazikika mtima pa maso pa mulungu. Ife timalandira chilichonse tipempha kwa iye, chifukwa timamvera malamulo ake ndi kuchita zimene zimamukondweretsa. Nthawi imene tichita izi; iye amakhala mwa ife ndipo ife timakhala mwa iye.  1 John 3:19-24, as we are strong hearted and stead fast before God, we are helped to realise that we stand in truth and we are at peace within our hearts before God. we receive all that we ask from God, because we listen to him and his commands and do all that he asks of us. All the time as we do this, he lives in us and we live in him. 

  • 40 min
  Chikondi pa wina ndi mnzake ndi m'choonadi/Love for one another and in truth

  Chikondi pa wina ndi mnzake ndi m'choonadi/Love for one another and in truth

  1 Yohane 3:11-18, mawu awa akutikumbutsa za chikondi chathu pa wina ndi mnzake makamaka pamene ife tsono ndi ake a mulungu, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa koma cha ntchito zathu ndi m'choonadi kuwonetsera chiyanjano chathu ndi mulungu wathu mwa ambuye wathu Yesu Khristu.  1 John 3:11-18, these words are reminding us of our love for one another especially now that we are children of God, our love for each other should not be in words only but in works also and in truth showing our fellowship with God through our lord Jesus Christ.  

  • 1 hr 8 min
  Ana A Mulungu/The Children Of God

  Ana A Mulungu/The Children Of God

  1 Yohane 2:28-3:1-10, mawu a mulungu awa akuthandiza onse omwe ndi ake mulungu kuzindikira kuti pamene ife tagulidwa ndi mwazi wake wa Yesu khristu ndife tsopano ana a mulungu. Ana a mulungu amachita chilungamo ndipo ndiwolungama. Onse omwe alimwa khristu amafanana naye iye. Koma ngati pakati pathu pali ena omwe sachita chilungamo ngakhalenso sakonda m'bale wawo, amenewo siake a mulungu koma a mdierekezi.

  1 John 2:28-3:1-10, these words of God are helping us all, children of God to realise that when we were bought by the blood of Christ Jesus, we became his. And now we are known as children of God. The children of God are evident by this fact that whoever does practice righteousness and is just belongs to God. But if one does not, even to love his brother becomes a problem for him then he is of the Devil.   

  • 47 min
  Khalani mwa Khristu/Remain in Christ

  Khalani mwa Khristu/Remain in Christ

  1 Yohane 2:18-27, nthawi zambiri anthu amafunsa kuti kodi 'tili nthawi ya masiku omaliza?' Yankho ndi eya. Nthawi ya masiku omaliza ndi pakati pa kubwera kwa Yesu Khristu koyamba ndi kubwera kwa Yesu Khristu kachiwiri. Bukuli likubweretsa poyera nkhani imene ndiyovuta kuyimvetsa. Kodi okana Khristu abwera liti? Paulo akunena motere pakhaniyi, okana Khristu wamkulu adzabwera koma chidwichathu chikhale apa, okana khristu ambiri afika kale. Ndipo ambiri alipakati pathu, mipingo mwadzadza ndi anthu oterewa. Funso nati, kodi ife tili mwa Khristu, kapena gawo lathu ndi lokana Khristu?  1 John 2:18-27, many times people ask in wonder, are we in the ladder days? The answer is yes. The time between the first coming of Jesus Christ an his second coming marks the end of times or the ladder days. This book brings to light about the most confusing story about the anti christ. About the anti christ, When is the anti christ coming? Paul tells us clear that the great anti christ is coming but our focus should be at the anti christ who are already here. many of them are among us, and in our midst they are rejecting christ. But the question still remains, are we remaining in christ or are we partaking the anti christ?   

  • 38 min
  Kondani Mulungu/Love God

  Kondani Mulungu/Love God

  1 Yohane 2:12-17,chifukwa chachikondi chimene tilinacho pa mulungu wathu, timamumvera ndi kutsatira malamulo ake. Choncho timawonetsera ku dziko lonse kuti ndife ake kudzera muchikondi chomwe tilinacho pa mulungu wathu. Ndichifukwa chake abale tiyeni tipitirize monga okhulupirira komanso okonda mulungu ndi kukana dziko lapansi.  1 John 2:12-17, because of the love we have for God, we continue to love him more. Through our faith, we continue to also obey his commandments. We continue to show the world that we belong to God and that we love him through our living as christians. It is also the reason why brothers, we should continue to love God and continue living as christians and denying the offers of the world.

  • 56 min
  Kumvera Mulungu ndi Malamulo ake/Obedient to God and his commandment

  Kumvera Mulungu ndi Malamulo ake/Obedient to God and his commandment

  1 Yohane 2:3-11, Buku la 1 Yohane likupitiriza kubwera poyera njira zomwe khristu opulumutsidwa akuyenera kupitiriza kuyenda pa nthawi imene khristu wapulumutsidwa. Kumvera mulungu ndi malamulo ake ndi chiwonetsero chachikulu ndi chilungamo chathu kwa anthu kuti ife timankonda mulungu, timakhulupirira mulungu wathu, zonse zimene mulungu atilamulira kuti tichite ife timamvera ndikuchita.  1 John 2:3-11, the book of 1 John continues to shade light on principles that true christians are continuously to show in the congregation and to the people who are not part of the church and are regarded as non believers. Obedient to God and his principles shows a sign and our justice to others that we love God and that we obey his principles and all that God commands us we willingly do.       

  • 58 min

Top Podcasts In Religion & Spirituality

Ascension
D-Group
Ascension
Hank Smith & John Bytheway
Joel Osteen
BibleProject Podcast